2 Kings 2:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo a m'gulu la aneneri amene anali ku Yeriko adadzakumana ndi Elisa, namufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti lero Chauta akulandani mbuyanu?” Elisa adayankha kuti, “Inde, ndikudziŵa, koma musakambe za zimenezi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ana a aneneri okhala ku Yeriko anayandikira kwa Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati iye, Inde ndidziwa, khalani muli chete.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana a aneneri amene anali ku Yeriko anapita kwa Elisa, namufunsa kuti, “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova akuchotsera mbuye wako?” Elisa anayankha kuti, “Inde ndikudziwa, koma inu musakambe zimenezi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ana a aneneri okhala ku Yeriko anayandikira kwa Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akucotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati iye, Inde ndidziwa, khalani muli cete.