2 Kings 2:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Eliya adauza Elisa kuti, “Iwe, chonde ubaakhala pano, poti ine Chauta wandituma kuti ndipite ku Yordani.” Koma Elisa adauza Eliyayo kuti, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine sindikusiyani konse.” Motero aŵiri onsewo adapitiriza ulendo wao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Eliya ananena naye, Ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yordani. Nati iye, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Napitirira iwo awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Eliya anati kwa Elisa, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Yorodani.” Elisa anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapitirira ulendo wawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Eliya ananena naye, Ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yordano, Nati iye, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Napitirira iwo awiri.