2 Kings 2:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Eliya adatenga mwinjiro wake naupinda, kenaka adamenya madzi ndi mwinjirowo. Tsono madziwo adapatukana, ena kwina ena kwina, mpaka aneneri aŵiriwo adaoloka pouma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Eliya anagwira chofunda chake, nachipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Eliya anatenga chovala chake nachipinda, napanda madzi ndi chovalacho. Madziwo anagawikana, ena kwina ena kwina, ndipo awiriwo anawoloka powuma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Eliya anagwira copfunda cace, nacipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma.