2 Kings 20:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hezekiya adaŵalandira anthuwo, naŵaonetsa nyumba yosungiramo zinthu zake, monga siliva, golide, zokometsera chakudya, mafuta onunkhira amtengowapatali, zida zonse zankhondo, ndiponso zonse zimene ankazisunga m'nyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse m'nyumbamo ndi mu ufumu wake wonse kamene sadaŵaonetse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hezekiya anawamvera, nawaonetsa nyumba yonse ya chuma chake, siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba ya zida zake, ndi zonse zopezeka pachuma pake; panalibe kanthu m'nyumba mwake, kapena m'ufumu wake wonse osawaonetsa Hezekiya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hezekiya analandira amithengawo ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Anawaonetsa siliva, golide, zonunkhiritsa zakudya ndi mafuta abwino kwambiri, zida zake zankhondo ndiponso china chilichonse chimene chinali mosungiramo zinthu zake. Panalibe chinthu mʼnyumba yake yaufumu kapena mu ufumu wake wonse chimene Hezekiya sanawaonetse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hezekiya anawamvera, nawaonetsa nyumba yonse ya cuma cace, siliva, ndi golidi, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba ya zida zace, ndi zonse zopezeka pacuma pace; panalibe kanthu m'nyumba mwace, kapena m'ufumu wace wonse osawaonetsa Hezekiya.