2 Kings 20:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mneneri Yesaya adapita kwa mfumu Hezekiya, namufunsa kuti, “Kodi anthu amene aja adakuuzani zotani, ndipo adaachokera kuti?” Hezekiya adayankha kuti, “Adaachokera ku dziko lakutali, ku Babiloni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yesaya mneneri anadza kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Anatani anthu awa? Anadza kwa inu kufumira kuti? Nati Hezekiya, Afumira dziko la kutali ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya namufunsa kuti, “Kodi anthu aja anakuwuzani zotani ndipo anachokera kuti?” Hezekiya anayankha kuti, “Anachokera ku dziko lakutali, ku Babuloni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yesaya mneneri anadza kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Anatani anthu awa? anadza kwa inu kufumira kuti? Nati Hezekiya, Afumira dziko la kutari ku Babulo.