2 Kings 20:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesaya adamufunsanso kuti, “Kodi m'nyumba mwanumo adaona chiyani?” Hezekiya adayankha kuti, “Adaona zonse za m'nyumba mwanga. Palibe ndi chinthu chimodzi chomwe chimene sindidaŵaonetse m'nyumba zanga zosungiramo chuma.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Anaona chiyani m'nyumba mwanu? Nati Hezekiya, Zonse za m'nyumba mwanga anaziona, palibe kanthu pachuma changa kosawaonetsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mneneriyo anafunsa kuti, “Kodi anaona chiyani mʼnyumba yanu yaufumu?” Hezekiya anayankha kuti, “Anaona china chilichonse mʼnyumba yanga yaufumu ndipo palibe ndi chinthu chimodzi chomwe chimene sindinawaonetse mʼnyumba zanga zosungiramo chuma.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Anaona ciani m'nyumba mwanu? Nati Hezekiya, Zonse za m'nyumba mwanga anaziona, palibe kanthu pacuma canga kosawaonetsa.