2 Kings 20:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
nthaŵi idzafika pamene zonse za m'nyumba mwanu ndi zonse zimene makolo anu adazisonkhanitsa mpaka lero lino, adzakulandani kupita nazo ku Babiloni. Sipadzatsalapo ndi kanthu kamodzi komwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, akudza masiku kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zokundika makolo ako mpaka lero, zidzatengedwa kunka ku Babiloni, kosasiyidwa kanthu konse, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, masiku akubwera ndithu pamene zonse za mʼnyumba yanu yaufumu, zonse zimene makolo anu anazisunga mpaka lero, zidzatengedwa kupita ku Babuloni. Palibe chimene chidzatsale, akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, akudza masiku kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zokundika makolo ako mpaka lero, zidzatengedwa kumka ku Babulo, kosasiyidwa kanthu konse, ati Yehova.