2 Kings 20:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ambiri mwa ana anu, obala inu nomwe adzatengedwa, ndipo adzaŵasandutsa adindo ofulidwa otumikira ku nyumba ya mfumu ku Babiloni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nadzatenga ena a ana ako otuluka mwa iwe, amene udzawabala, nadzakhala iwo adindo m'chinyumba cha mfumu ya Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ena mwa ana anu omwe, amene mudzabereke adzatengedwa ndipo adzawasandutsa anthu ofulidwa mʼnyumba yaufumu ya mfumu ya Babuloni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nadzatenga ena a ana ako oturuka mwa iwe, amene udzawabala, nadzakhala iwo adindo m'cinyumba ca mfumu ya Babulo.