2 Kings 20:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Hezekiya adauza Yesaya kuti, “Mau amene Chauta walankhulaŵa ngabwino.” Ponena zimenezo, Hezekiya ankaganiza kuti, “Palibe kanthu ai, malinga kuti padzakhale mtendere ndi bata masiku onse a moyo wanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova udawanena ndi abwino. Natinso, Si momwemo nanga, mtendere ndi choonadi zikakhala masiku anga?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hezekiya anayankha kuti, “Mawu a Yehova amene mwayankhulawa ndi abwino. Pakuti iye ankaganiza kuti, ‘Kodi pa nthawi yanga sipadzakhala mtendere ndi bata?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova udawanena ndi abwino. Natinso, Si momwemo nanga, mtendere ndi coonaeli zikakhala masiku anga?