2 Kings 20:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Inu Chauta, mukumbukire kuti ndakhala ndikukutumikirani mokhulupirika ndi modzipereka. Ndipo nthaŵi zonse ndinali kuchita zokukomerani.” Atatero adayamba kulira ndi mtima woŵaŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukumbukire Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'choonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kuchita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu Yehova, kumbukirani ndithu mmene ndayendera mokhulupirika ndi mtima wonse ndipo ndachita zolungama pamaso panu.” Hezekiya analira kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukumbukile Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'coonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kucita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukuru.