2 Kings 20:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ndidzakuwonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako. Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzindawu kwa mfumu ya ku Asiriya. Mzindawu ndidzautchinjiriza chifukwa cha ulemu wanga ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndakuonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu; ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'dzanja la mfumu ya Asiriya; ndidzatchinjiriza mudzi uno, chifukwa cha Ine ndekha, ndi chifukwa cha Davide mtumiki wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako. Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzinda umenewu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya. Ndidzateteza mzinda umenewu chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndakuonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu; ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'dzanja la mfumu ya Asuri; ndidzacinjiriza mudzi uno, cifukwa ca Ine ndekha, ndi cifukwa ca Davide mtumiki wanga.