2 Kings 20:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Hezekiya adafunsa Yesaya uja kuti, “Kodi padzakhala chizindikiro chanji choonetsa kuti Chauta adzandichiritsa, ndipo kuti ndidzatha kukapembedza ku Nyumba ya Chauta mkucha uno?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Hezekiya kwa Yesaya, Chizindikiro chake nchiyani kuti Yehova adzandichiza, ndi kuti ndidzakwera kunka kunyumba ya Yehova tsiku lachitatu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Hezekiya anafunsa Yesaya kuti, “Kodi padzakhala chizindikiro chanji choonetsa kuti Yehova adzandichiritsa ndi kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova pa tsiku lachitatu kuchokera lero lino?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Hezekiya kwa Yesaya, Cizindikilo cace nciani kuti Yehova adzandiciza, ndi kuti ndidzakwera kumka ku nyumba ya Yehova tsiku lacitatu?