2 Kings 21:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Manase mfumu ya ku Yuda wachita zonyansa zambiri, ndipo wachita zoipa kupambana zoipa zonse zimene ankachita Aamori amene adaalipo kale iye asanabadwe, ndipo wachimwitsanso anthu a ku Yuda ndi mafano akewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza Manase mfumu ya Yuda anachita zonyansa izi, pakuti zoipa zake zinaposa zonse adazichita Aamori, amene analipo asanabadwe iye, nalakwitsanso Yuda ndi mafano ake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Manase mfumu ya Yuda wachita machimo onyansawa ndipo wachita zoyipa kupambana Aamori amene analipo kale iye asanabadwe ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda ndi mafano ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza Manase mfumu ya Yuda anacita zonyansa izi, pakuti zoipa zace zinaposa zonse adazicita Aamori, amene analipo asanabadwe iye, nalakwitsanso Yuda ndi mafano ace;