2 Kings 21:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti, ‘Ndithu, ndidzabweretsa pa Yerusalemu ndi pa Yuda choipa chakuti aliyense amene adzachimve, adzadodoma nkupukusa mutu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake atero Yehova Mulungu wa Israele, Taonani, nditengera Yerusalemu ndi Yuda choipa, chakuti yense achimvera chidzamliritsa mwini khutu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Taonani, ndikubweretsa pa Yerusalemu ndi Yuda mavuto akuti aliyense amene adzawamve adzathedwa nzeru.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Taonani, nditengera Yerusalemu ndi Yuda coipa, cakuti yense acimvera cidzamliritsa mwini khutu.