2 Kings 21:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzalanga Yerusalemu monga ndidalangira Samariya ndi Ahabu, pamodzi ndi banja lake. Tsono ndidzayeretsa Yerusalemu pochotsa anthu ake, monga momwe munthu amachitira popukuta mbale, ndipo ataipukuta amaivundikira pansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzayesa pa Yerusalemu chingwe choongolera cha Samariya, ndi chingwe cholungamitsira chilili cha nyumba ya Ahabu; ndidzapukuta Yerusalemu monga umo apukutira mbale, kuipukuta ndi kuivundikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzalanga Yerusalemu ndi Yuda pogwiritsa ntchito muyeso umene ndinalangira Samariya ndi Ahabu pamodzi ndi nyumba yake. Ndidzayeretsa Yerusalemu monga mmene munthu amachitira popukuta mbale ndipo atayipukuta amayivundikira pansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzayesa pa Yerusalemu cingwe coongolera ca Samariya, ndi cingwe colungamitsira ciriri ca nyumba ya Ahabu; ndidzapukuta Yerusalemu monga umo apukutira mbale, kuipukuta ndi kuibvundikira.