2 Kings 21:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu otsala ndidzaŵachotsa m'dziko ndi kuŵapereka m'manja mwa adani ao. Adzaphedwa ndipo adaniwo adzaŵalanda zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzataya chotsala cha cholowa changa, ndi kuwapereka m'dzanja la adani ao, nadzakhala iwo chakudya ndi chofunkha cha adani ao onse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawataya anthu otsala amene ndi cholowa changa ndipo ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo. Adzachotsedwa ndipo adaniwo adzawalanda zinthu zonse
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzataya cotsala ca colowa canga, ndi kuwapereka m'dzanja la adani ao, nadzakhala iwo cakudya ndi cofunkha ca adani ao onse;