2 Kings 21:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Manase uja adakhetsa kwambiri magazi a anthu osachimwa, mpaka magaziwo kuyenderera m'miseu ya Yerusalemu kuyambira mbali ina mpaka mbali ina. Izi zidaonjezera pa machimo amene adachimwitsa nawo Ayuda pakuŵachititsa zoipa zonyoza Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosachimwa mpaka anadzaza m'Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwake analakwitsa nako Yuda, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuwonjezera apo, Manase anakhetsa kwambiri magazi a anthu osalakwa mpaka magaziwo kuyenderera mu Yerusalemu kuyambira mbali ina mpaka mbali ina, kuphatikiza pa kuchimwitsa Yuda, kotero kuti anthu anachita zoyipa pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosacimwa mpaka anadzaza m'Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwace analakwitsa nako Yuda, ndi kucita coipa pamaso pa Yehova.