2 Kings 21:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo adachita zoipa pamaso pa Chauta, potsata ntchito zonyansa za anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵapirikitsa pofika Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, potsatira mchitidwe wonyansa wa mitundu imene Yehova anayipirikitsa pofika Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israyeli.