2 Kings 21:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthu am'dzikomo adapha onse aja amene adamchita chiwembu mfumu Amoniyo. Kenanaka anthuwo adalonga Yosiya mwana wake kuti akhale mfumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anthu a m'dzikomo anapha onse akumchitira chiwembu mfumu Amoni; ndipo anthu a m'dzikomo anamlonga ufumu Yosiya mwana wake m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthu a mʼdzikomo anapha onse amene anachitira chiwembu Mfumu Amoni, nayika Yosiya mwana wake kukhala mfumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anthu a m'dzikomo anapha onse akumcitira ciwembu mfumu Amoni; ndipo anthu a m'dzikomo anamlonga ufumu Yosiya mwana wace m'malo mwace.