2 Kings 21:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Manaseyo adamanganso akachisi amene bambo wake Hezekiya adaaononga ku mapiri. Adamangira Baala maguwa, napanga mafano monga m'mene ankachitira Ahabu mfumu ya Aisraele. Ndipo ankapembedza zinthu zakuthambo namazitumikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti anamanganso misanje, imene Hezekiya atate wake adaiononga; nautsira Baala maguwa a nsembe, nasema chifanizo, monga anachita Ahabu mfumu ya Israele, nagwadira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iyetu anamanganso malo opembedzera mafano amene Hezekiya abambo ake anawawononga. Anamangira Baala maguwa a nsembe ndi mtengo wa fano la Asera monga anachitira Ahabu mfumu ya Israeli ndipo ankapembedza zolengedwa zonse zamlengalenga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti anamanganso misanje, imene Hezekiya atate wace adaiononga; nautsira Baala maguwa a nsembe, nasema cifanizo, monga anacita Ahabu mfumu ya Israyeli, nagwadira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.