2 Kings 21:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adapereka mwana wake wamwamuna ngati nsembe. Ankatama mizimu mopemba ndiponso ankaombeza maula, namachita zobwebwetetsa ndi zaufiti. Adachita zoipa zambiri zimene zidakwiyitsa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Napititsa mwana wake pamoto, naombeza maula, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anapsereza mwana wake pa moto ngati nsembe, ankachita za matsenga, ankawombeza mawula, ankapita kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ndiponso ankapembedza mizimu. Iyeyo anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova ndipo anakwiyitsa Yehovayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Napititsa mwana wace pamoto, naombeza maula, nacita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anacita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wace.