2 Kings 21:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaika m'Nyumba ya Chauta fano losema la Asera. Nyumba imeneyo, Chauta anali atauza Davide ndi Solomoni mwana wake kuti, “M'nyumba iyi ndi mu Yerusalemu muno, ndimo m'mene ndasankha pakati pa mafuko onse a Israele kuti azindipembedzeramo mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaika chifanizo chosema chimene adachipanga m'nyumba ija Yehova adainenera kwa Davide ndi kwa Solomoni mwana wake kuti, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha mwa mafuko onse a Israele ndidzaikamo dzina langa kosatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anatenga fano losema la Asera limene analipanga ndi kuliyika mʼNyumba ya Yehova, Nyumba imene Yehova ananena kwa Davide ndi mwana wake Solomoni kuti, “Mʼnyumba iyi ndi mu Yerusalemu ndiwo malo amene ndasankha pakati pa mafuko onse a Aisraeli kuyikamo Dzina langa kwamuyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaika cifanizo cosema cimene adacipanga m'nyumba ija Yehova adainenera kwa Davide ndi kwa Solomo mwana wace kuti, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha mwa mafuko onse a Israyeli ndidzaikamo dzina langa kosatha.