2 Kings 21:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono sindidzalola kuti Aisraele adzachotsedwe m'dziko lao limene ndidapatsa makolo ao, malinga kuti iwowo azisamala kuchita zinthu zonse motsata Malamulo amene ndaŵalamula, ndiponso motsata Malamulo amene Mose mtumiki wanga adaŵalamula.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo sindidzachotsanso mapazi a Israele m'dziko ndidalipereka kwa makolo ao; chokhachi asamalire kuchita monga mwa zonse ndawalamulira ndi monga mwa chilamulo chonse anawalamulira Mose mtumiki wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sindidzalola kuti Aisraeli achotsedwe mʼdziko lawo limene ndinapatsa makolo awo ngati iwowo adzasamala kuchita zinthu zonse zimene ndinawalamula ndi kusunga malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anawapatsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo sindidzacotsanso mapazi a Israyeli m'dziko ndidalipereka kwa makolo ao; cokhaci asamalire kucita monga mwa zonse ndawalamulira ndi monga mwa cilamulo conse anawalamulira Mose mtumiki wanga.