2 Kings 22:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosiya anali wa zaka zisanu ndi zitatu pamene adadaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 31 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yedida mwana wa Adaya wa ku Bozikati.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu chimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndi Yedida mwana wa Adaya wa ku Bozikati.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosiya anakhala mfumu ali ndi zaka zisanu ndi zitatu ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 31. Amayi ake anali Yedida mwana wa Adaiya wochokera ku Bozikati.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu cimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndi Yedida mwana wa Adaya wa ku Bozikati.