2 Kings 22:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pitani mukafunse Chauta m'malo mwanga ndi m'malo mwa anthu a m'dziko lonse la Yuda, za mau a m'buku limene lapezekali. Ndithu mkwiyo wa Chauta umene watiyakirawu ngwaukulu, chifukwa choti makolo athu sadamvere mau a m'bukuli, ndipo sadatsate zonse zimene zidalembedwa m'menemo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukani, funsirani ine, ndi anthu, ndi Yuda yense, kwa Yehova za mau a buku ili adalipeza; pakuti mkwiyo wa Yehova wotiyakira ife ndi waukulu; popeza atate athu sanamvere mau a buku ili, kuchita monga mwa zonse zotilemberamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pitani mukafunse Yehova mʼmalo mwanga ndi mʼmalo mwa anthu onse a mʼdziko la Yuda, za zomwe zalembedwa mʼbuku limene lapezekali. Mkwiyo wa Yehova ndi waukulu kwambiri pa ife ndipo watiyakira chifukwa makolo athu sanamvere mawu a buku ili. Iwo sanachite molingana ndi zonse zimene zalembedwa mʼmenemu zokhudza ife.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukani, funsirani ine, ndi anthu, ndi Yuda yense, kwa Yehova za mau a buku ili adalipeza; pakuti mkwiyo wa Yehova wotiyakira ife ndi waukuru; popeza atate athu sanamvera mau a buku ili, kucita monga mwa zonse zotilemberamo.