2 Kings 22:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero wansembe Hilikiya, Ahikamu, Akibori, Safani ndi Asaya adapita kwa mneneri wamkazi dzina lake Hulida, mkazi wa Salumu. Salumuyo, wosunga zovala zachifumu anali mwana wa Tikiwa, mwana wa Harihasi. Mkaziyu ankakhala ku Yerusalemu m'dera latsopano la mzindawo. Tsono anthu aja atalankhula naye,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Namuka Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu, ndi Akibori, ndi Safani, ndi Asaya, kwa Hulida mneneri wamkazi, ndiye mkazi wa Salumu mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi, wosunga zovala za mfumu; analikukhala iye m'Yerusalemu m'dera lachiwiri, nalankhula naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Hilikiya wansembe, Ahikamu, Akibo, Safani ndi Asaiya anapita kukayankhula ndi Hulida, mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi, wosunga zovala zaufumu. Mneneri wamkaziyu ankakhala mu Yerusalemu, ku chigawo chachiwiri cha mzindawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Namuka Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu, ndi Akibori, ndi Safani, ndi Asaya, kwa Hulida mneneri wamkazi, ndiye mkazi wa Salumu mwana wa Tlkiva, mwana wa Harasi, wosunga zobvala za mfumu; analikukhala iye m'Yerusalemu m'dera laciwiri, nalankhula naye.