2 Kings 22:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chakuti anthuwo andisiya Ine namafukiza lubani kwa milungu ina, nkumandichimwira ndi mafano ao, ntchito zonse za manja ao, Ine pano mkwiyo wanga wayakira mzinda uno ndipo sudzazima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza anandisiya Ine, nafukizira zonunkhira milungu ina, kuti autse mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao; chifukwa chake mkwiyo wanga udzayakira malo ano wosazimikanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa anthuwo andisiya Ine ndi kumafukiza lubani kwa milungu ina nandikwiyitsa ndi mafano onse amene manja awo anapanga, mkwiyo wanga udzayaka pa malo ano ndipo sudzazimitsidwa.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza anandisiya Ine, nafukizira zonunkhira milungu yina, kuti autse mkwiyo wanga ndi nchito zonse za manja ao; cifukwa cace mkwiyo wanga udzayakira malo ana wosazimikanso.