2 Kings 22:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pakuti mtima wako walapa ndipo wadzichepetsa pamaso pa Ine Chauta, utamva mau amene ndidalankhula otsutsa mzinda uno ndi anthu onse okhala m'menemo. Ndithudi mzinda uno udzakhala bwinja ndi malo otembereredwa. Popeza kuti wang'amba zovala zako numalira pamaso panga, Inenso ndamva pemphero lako, ndatero Ine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza mtima wako ngoolowa, ndipo unadzichepetsa pamaso pa Yehova muja udamva zonenera Ine malo ano ndi anthu okhalamo, kuti adzakhala abwinja, ndi temberero; ndipo unang'amba zovala zako ndi kulira misozi pamaso panga, Inenso ndakumvera, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa unasweka mtima ndi kudzichepetsa wekha pamaso pa Yehova, pamene unamva zomwe zinayankhulidwa zotsutsana ndi malo ano ndi anthu ake, kuti adzakhala otembereredwa nasanduka bwinja, ndiponso chifukwa unangʼamba zovala ndi kulira pamaso panga, ndamva pemphero lako, akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza mtima wako ngoolowa, ndipo unadzicepetsa pamaso pa Yehova muja udamva zonenera Ine malo ana ndi anthu okhalamo, kuti adzakhala abwinja, ndi temberero; ndipo unang'amba zobvala zako ndi kulira misozi pamaso panga, Inenso ndakumvera, ati Yehova.