2 Kings 22:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Ine ndidzakutenga, iweyo ukalondole makolo ako ndipo udzaikidwa m'manda mwamtendere. Motero maso ako sadzaona zoipa zija zimene ndidzabweretsa pa mzinda uno.’ ” Tsono anthu aja adabwerera nakanena mau amenewo kwa mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, taona, ndidzakusonkhanitsa ukhale ndi makolo ako, nudzatengedwa ulowe m'manda mwako mumtendere; ndipo sudzaona m'maso mwako choipa chonse ndidzachifikitsira malo ano. Ndipo anambwezera mfumu mau.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho taona, Ine ndidzakutenga kupita kwa makolo ako ndipo udzayikidwa mʼmanda mwako mwamtendere. Maso ako sadzaona mavuto onse amene ndidzabweretse pamalo pano.’ ” Ndipo anthu aja anabwerera nakafotokoza mawu amenewa kwa mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, taona, ndidzakusonkhanitsa ukhale ndi makolo ako, nudzatengedwa ulowe m'manda mwako mumtendere; ndipo sudzaona m'maso mwako coipa conse ndidzacifikitsira malo ano. Ndipo anambwezera mfumu mau.