2 Kings 22:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pita kwa Hilikiya, mkulu wa ansembe, ukamuuze kuti aŵerenge ndalama zimene anthu abwera nazo ku Nyumba ya Chauta, zimene alonda apakhomo adasonkhanitsa kwa anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwera kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, awerenge ndalama zimene anthu anabwera nazo kunyumba ya Yehova, ndizo zimene olindira pakhomo anasonkhetsa anthu; azipereke m'dzanja la antchito akuyang'anira nyumba ya Yehova;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pita kwa mkulu wa ansembe Hilikiya ndipo ukamuwuze kuti awerenge ndalama zimene anthu abwera nazo ku Nyumba ya Yehova, zimene alonda a pa khomo anasonkhanitsa kwa anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwera kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, awerenge ndalama zimene anthu anabwera nazo ku nyumba ya Yehova, ndizo zimene olindira pakhomo anasonkhetsa anthu; azipereke m'dzanja anchito akuyang'anira nyumba ya Yehova;