2 Kings 22:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye kuti alipire amisiri a matabwa, amisiri omanga nyumba, amisiri omanga ndi miyala ndiponso amene adapereka mitengo ndi miyala yosema yokonzera Nyumbayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kwa amisiri a mitengo, ndi omanga nyumba, ndi omanga linga; ndi kuti agule mitengo ndi miyala yosema kukonza nazo nyumbayi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
amisiri a matabwa, amisiri omanga ndi amisiri a miyala. Iwo akagulenso matabwa ndi miyala yosemedwa kuti akonzere Nyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kwa amisiri a mitengo, ndi omanga nyumba, ndi omanga linga; ndi kuti agule mitengo ndi miyala yosema kukonza nazo nyumbayi.