2 Kings 22:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Hilikiya, mkulu wa nsembe uja, adauza Safani, mlembi uja, kuti, “Ndalipeza buku la Malamulo lija m'Nyumba ya Chauta.” Ndipo Hilikiya adapereka bukulo kwa Safani, iye naliŵerenga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hilikiya mkulu wa ansembe anati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la chilamulo m'nyumba ya Yehova. Napereka Hilikiya bukulo kwa Safani, iye naliwerenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkulu wa ansembe Hilikiya anawuza Safani, mlembiyo kuti, “Ndapeza Buku la Malamulo mʼNyumba ya Yehova.” Anapereka bukulo kwa Safani amene analiwerenga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hilikiya mkulu wa ansembe anati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la cilamulo m'nyumba ya Yehova. Napereka Hilikiya bukulo kwa Safani, iye naliwerenga.