2 Kings 23:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Yosiya adaononganso ng'anjo yotchedwa Tofeti imene inali m'chigwa cha ana a Hinomu, kuti munthu aliyense asapereke mwana wake wamwamuna kapena wamkazi ngati nsembe kwa Moleki.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anawaipitsiranso Tofeti, wokhala m'chigwa cha ana a Hinomu; kuti asapitirize mmodzi yense mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pamoto kwa Moleki.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Yosiya anawononganso Tofeti, amene anali ku Chigwa cha Hinomu, kuti wina aliyense asagwiritse ntchito malowo popereka mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pa moto kwa Moleki.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anawaipitsiranso Tofeti, wokhala m'cigwa ca ana a Hinomu; kuti asapitirize mmodzi yense mwana wace wamwamuna kapena wamkazi pamoto kwa Moleki.