2 Kings 23:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adachotsanso akavalo amene mafumu a ku Yuda adaaŵapereka ngati nsembe kwa dzuŵa. Akavalo amenewo ankaŵasunga pa bwalo la Nyumba ya Mulungu pafupi ndi chipata choloŵera m'Nyumbamo, ndiponso chipinda cha Natani Meleki, mkulu wosunga nyumbayo. Kenaka adatentha magaleta opembedzera dzuŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nachotsanso akavalo amene mafumu a Yuda adapereka kwa dzuwa, polowera nyumba ya Yehova, ku chipinda cha Natani-Meleki mdindoyo, chokhala kukhonde; natentha magaleta a dzuwa ndi moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anachotsa pa chipata cholowera ku Nyumba ya Yehova akavalo amene mafumu a Yuda anawapereka ngati nsembe kwa dzuwa. Akavalo anali pafupi ndi bwalo la chipinda cha mkulu wina wotchedwa Natani-Meleki. Ndipo Yosiya anatentha magaleta opembedzera dzuwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nacotsanso akavalo amene mafumu a Yuda adapereka kwa dzuwa, polowera nyumba ya Yehova, ku cipinda ca Natani Meleki mdindoyo, cokhala kukhonde; natentha magareta a dzuwa ndi moto.