2 Kings 23:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mfumuyo idagwetsa ndi kuphwanyaphwanya maguwa a pa denga la chipinda chapamwamba cha Ahazi, amene adaŵamanga mafumu a ku Yuda, ndiponso maguwa amene Manase adaŵamanga pa mabwalo aŵiri a Nyumba ya Chauta. Ndipo adataya fumbi lake mu mtsinje wa Kidroni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi maguwa a nsembe anali patsindwi pa chipinda chosanja cha Ahazi adawapanga mafumu a Yuda, ndi maguwa a nsembe adawapanga Manase m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova, mfumu inawagumula, niwachotsa komweko, nitaya fumbi lao ku mtsinje wa Kidroni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anagwetsa maguwa amene mafumu a Yuda anawamanga pa denga pafupi ndi chipinda chapamwamba cha Ahazi, ndiponso maguwa amene Manase anamanga mʼmabwalo awiri a Nyumba ya Yehova. Yosiya anawachotsa kumeneko nawaphwanya ndi kutaya zidutswa zake mʼChigwa cha Kidroni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi maguwa a nsembe anali patsindwi pa cipinda cosanja ca Ahazi adawapanga mafumu a Yuda, ndi maguwa a nsembe adawapanga Manase m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova, mfumu inawagumula, niwacotsa komweko, nitaya pfumbi lao ku mtsinje wa Kidroni.