2 Kings 23:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mfumuyo idaononganso akachisi opembedzerapo mafano amene anali kuvuma kwa Yerusalemu, kumwera kwa phiri lotchedwa Chiwonongeko. Maguwawo Solomoni, mfumu ya ku Israele, adaaŵamangira fano lonyansa la Asidoni lotchedwa Asitoreti, ndi la Amowabu lotchedwa Kemosi, ndiponso la Aamoni lotchedwa Milikomu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inawaipitsira misanje yokhala kum'mawa kwa Yerusalemu, ndiyo ya ku dzanja lamanja la phiri la chionongeko, imene Solomoni mfumu ya Israele adaimangira Asitoreti chonyansa cha Asidoni, ndi Kemosi chonyansa cha Mowabu, ndi Milikomu chonyansa cha ana a Amoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumuyo inawononga malo opembedzera mafano amene ali kummawa kwa Yerusalemu cha kumpoto kwa Phiri la Chiwonongeko. Maguwawa Solomoni mfumu ya Israeli inamangira Asitoreti, fano lalikazi lonyansa la Asidoni, Kemosi, fano lonyansa la Amowabu, ndi Moleki, fano lonyansa la anthu a ku Amoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inawaipitsira misanje yokhala kum'mawa kwa Yerusalemu, ndiyo ya ku dzanja lamanja la phiri la cionongeko, imene Solomo mfumu ya Israyeli adaimangira Asitoreti conyansa ca Asidoni, ndi Kemosi conyansa ca Moabu, ndi Milikomu conyansa ca ana a Amoni.