2 Kings 23:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosiya adagwetsanso guwa la ku Betele, limene Yerobowamu, mwana wa Nabati, adaalimanga ku kachisi pa chitunda. Yerobowamuyo adaachimwitsa Aisraele ndi guwa limenelo. Ndipo Yosiya adagumula guwalo naphwanyanso miyala yake, nkuiperapera, naisandutsa fumbi. Adatenthanso kachisiyo, pamodzi ndi mafano a Asera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anagumulanso guwa la nsembe linali ku Betele, ndi msanje adaumanga Yerobowamu mwana wa Nebati wolakwitsa Israele uja; guwa la nsembelo, ndi msanje womwe anagumula; natentha msanje, naupondereza ukhale fumbi, natentha chifanizo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhalenso guwa lansembe la ku Beteli, malo opembedzera mafano amene anapanga Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa Israeli, Yosiya anawononga guwalo ndi malo opembedzera mafanowo. Iye anatentha malo opembedzera mafanowo ndi kuwapera ndipo anatenthanso fano la Asera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anagumulanso guwa la nsembe linali ku Beteli, ndi msanje adaumanga Yerobiamu mwana wa Nebati wolakwitsa Israyeli uja; guwa la nsembelo, ndi msanje womwe anagumula; natentha msanje, naupondereza ukhale pfumbi, natentha cifanizoco.