2 Kings 23:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atatero, Yosiya adacheuka naona manda paphiripo. Tsono adatuma anthu kuti akatenge mafupa m'mandamo, ndipo adaŵatenthera paguwapo. Potero adalidetsa monga momwe Chauta adaanenera kudzera mwa mneneri wake amene adaaloseratu zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo potembenuka Yosiya anaona manda okhalako kuphiri, natumiza anthu natulutsa mafupa kumanda, nawatentha pa guwa la nsembe, kuliipitsa, monga mwa mau a Yehova anawalalikira munthu wa Mulungu wolalikira izi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yosiya anayangʼanayangʼana ndipo ataona manda amene anali pomwepo, mʼmbali mwa phiri, analamula kuti afukule mandawo ndi kutulutsa mafupa kuti awatenthe paguwapo kuti alidetse, potsatira mawu a Yehova amene munthu wa Mulungu analoseratu za zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo potembenuka Yosiya anaona manda okhalako kuphiri, natumiza anthu naturutsa mafupa kumanda, nawatentha pa guwa la nsembe, kuliipitsa, monga mwa mau a Yehova anawalalikira munthu wa Mulungu wolalikira izi.