2 Kings 23:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mfumu idafunsa kuti, “Kodi manda ena ndikuwona apowo ngayani?” Anthu amumzindamo adamuuza kuti, “Amenewo ndi manda a mneneri wa Mulungu wa ku Yuda amene adaneneratu za zimene inu mwalichita guwa la ku Betele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anatinso, Chizindikiro ichi ndichiona nchiyani? Namuuza anthu a m'mudziwo, Ndicho manda a munthu wa Mulungu anafuma ku Yuda, nalalikira izi mwazichitira guwa la nsembe la ku Betele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inafunsa kuti, “Kodi chizindikiro cha manda chimene ndikuwaonawo ndi chayani?” Anthu a mu mzindamo anayankha kuti, “Ndi chizindikiro cha manda a munthu wa Mulungu wochokera ku Yuda amene ananeneratu zimene inu mwalichita guwa lansembe la Beteli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anatinso, Cizindikilo ici ndiciona nciani? Namuuza anthu a m'mudziwo, Ndico manda a munthu wa Mulungu anafuma ku Yuda, nalalikira izi mwazicitira guwa la nsembe la ku Beteli.