2 Kings 23:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosiyayo adaononganso nyumba zonse zopembedzeramo mafano zija zimene zinali m'mizinda ya ku Samariya. Mafumu a ku Israele ndiwo amene adaamanga zimenezi, naputa mkwiyo wa Chauta potero. Yosiya uja adachita chimodzimodzi kumeneko monga momwe adaachitira ku Betele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi nyumba zonse zomwe za ku misanje yokhala m'midzi ya Samariya, adazimanga mafumu a Israele kuutsa nazo mkwiyo wa Yehova, Yosiya anazichotsa, nazichitira monga mwa ntchito zonse adazichita ku Betele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga momwe Yosiya anachitira ku Beteli, anachotsa ndi kuwononga nyumba za milungu zonse ndi malo opembedzera mafano amene mafumu anamanga mʼmizinda ya ku Samariya omwe anakwiyitsa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi nyumba zonse zoo mwe za ku misanje yokhala m'midzi ya Samariya, adazimanga mafumu a Israyeli kuutsa nazo mkwiyo wa Yehova, Yosiya anazicotsa, nazicitira monga mwa nchito zonse adazicita ku Beteli.