2 Kings 23:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo mfumuyo idapita ku Nyumba ya Chauta pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, nzika zonse za mu Yerusalemu, ansembe ndi aneneri, ndiponso anthu onse aakulu ndi aang'ono omwe. Tsono iye adaŵerenga pamaso pao mau onse a m'buku lija la chipangano limene lidaapezeka m'Nyumba ya Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nikwera mfumu kunka kunyumba ya Yehova, ndi amuna onse a Yuda, ndi onse okhala m'Yerusalemu pamodzi naye, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi anthu onse ang'ono ndi akulu; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a m'buku la chipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumuyo inapita ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu, ansembe ndi aneneri, ndiponso anthu ena onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. Mfumuyo inawerenga mawu onse a mʼBuku la Chipangano limene linapezeka mʼNyumba ya Yehova, anthu onse akumva.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nikwera mfumu kumka ku nyumba ya Yehova, ndi amuna onse a Yuda, ndi onse okhala m'Yerusalemu pamodzi nave, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi anthu onse ang'ono ndi akulu; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a m'buku la cipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova.