2 Kings 23:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapha ansembe onse amene ankatumikira ku nyumba zochipembedzeramo mafano kumeneko. Adaŵaphera pa maguwa ao, natentha mafupa a anthuwo pamaguwapo. Pambuyo pake adabwerera ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapha ansembe onse a misanje okhalako pa maguwa a nsembe, natentha mafupa a anthu pamenepo, nabwerera kunka ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosiya anapha ansembe onse amene ankatumikira ku malo opembedzera mafano, anawaphera pa maguwa awo ndi kutentha mafupa awo. Kenaka iye anapita ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapha ansembe onse a misanje okhalako pa maguwa a nsembe, natentha-mafupa a anthu pamenepo, nabwerera kumka ku Yerusalemu.