2 Kings 23:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paska yotereyi inali isanachitikepo kuyambira nthaŵi ya aweruzi amene ankatsogolera Aisraele, kapena nthaŵi ya mafumu a ku Israele, kapenanso nthaŵi ya mafumu a ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zedi silinachitika Paska lotere chiyambire masiku a oweruza anaweruza Israele, ngakhale m'masiku a mafumu a Israele, kapena mafumu a Yuda;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paska yotere inali isanachitikepo kuyambira nthawi ya oweruza amene anatsogolera Israeli, kapenanso nthawi yonse ya mafumu a Yuda sipanachitikenso Paska ngati imeneyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zedi silinacitika Paskha lotere ciyambire masiku a oweruza anaweruza Israyeli, ngakhale m'masiku a mafumu a Israyeli, kapena mafumu a Yuda;