2 Kings 23:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku amenewo Yosiya adachotsanso anthu amaula, amatsenga, milungu ya m'nyumba ndiponso mafano ena onse, kudzanso zonyansa zonse zimene zinali ku dziko la Yuda ndi ku Yerusalemu. Adachita zimenezi kuti atsate Malamulo amene adalembedwa m'buku lomwe wansembe Hilikiya adalipeza m'Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso obwebweta, ndi openda, ndi aterafi, ndi mafano, ndi zonyansa zonse zidaoneka m'dziko la Yuda ndi m'Yerusalemu, Yosiya anazichotsa; kuti alimbitse mau a chilamulo olembedwa m'buku adalipeza Hilikiya wansembe m'nyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuwonjezera apa, Yosiya anachotsa anthu a mawula, woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, milungu ya mʼnyumba, mafano ndiponso zinthu zonse zonyansa zopezeka mu Yuda ndi Yerusalemu. Iye anachita izi pokwaniritsa lamulo lolembedwa mʼbuku limene Hilikiya analipeza mʼNyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso obwebweta, ndi openda, ndi aterafi, ndi mafano, ndi zonyansa zonse zidaoneka m'dziko la Yuda ndi m'Yerusalemu, Yosiya anazicotsa; kuti alimbitse mau a cilamulo olembedwa m'buku adalipeza Hilikiya wansembe m'nyumba ya Yehova.