2 Kings 23:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Chauta adati, “Ngakhale anthu a ku Yuda omwe, ndidzaŵachotsa pamaso panga, monga momwe ndachotsera anthu a ku Israele. Ndidzagwetsa ngakhale mzinda uno wa Yerusalemu umene ndidausankha, pamodzi ndi Nyumba imene ndidati, ‘Dzina langa lidzakhala m'menemo.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Yehova, Ndidzachotsa Yudanso pamaso panga, monga umo ndinachotsera Israele; ndipo ndidzataya mudzi uwu ndidausankha, ndiwo Yerusalemu, ndi nyumba ndidainena, Dzina langa lidzakhala komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehova anati, “Ndidzawachotsanso anthu a ku Yuda pamaso panga monga ndinachotsera anthu a ku Israeli ndipo ndidzawukana mzinda wa Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha, pamodzi ndi Nyumba ino imene ndinati, ‘Dzina langa lidzakhala mʼmenemo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Yehova, Ndidzacotsa Yudanso pamaso panga, monga umo ndinacotsera Israyeli; ndipo ndidzataya mudzi uwu ndidausankha, ndiwo Yerusalemu, ndi nyumba ndidainena, Dzina langa lidzakhala komweko.