2 Kings 23:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa masiku akewo Farao Neko, mfumu ya ku Ejipito, adapita kukathandiza mfumu ya ku Asiriya ku mtsinje wa Yufurate. Mfumu Yosiya adapita kukamenyana naye nkhondo. Koma Farao Neko adamupha Yosiyayo ku Megido pa nkhondoyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku ake Farao Neko mfumu ya Aejipito anakwerera mfumu ya Asiriya ku mtsinje wa Yufurate; ndipo mfumu Yosiya anatuluka kuponyana naye, koma anapha Yosiya ku Megido, atamuona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosiya akanali mfumu, Farao wotchedwa Neko, mfumu ya Igupto, anapita ku Mtsinje wa Yufurate kukathandiza mfumu ya ku Asiriya. Mfumu Yosiya anapita kukachita naye nkhondo, koma Neko anakumana naye ndi kumupha ku Megido.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku ace Farao-Neko mfumu ya Aigupto anakwerera mfumu ya Asuri ku mtsinje wa Firate; Ddipo mfumu Yosiya anaturuka kuponyana naye, koma anapha Yosiya ku Megido, atamuona.