2 Kings 23:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka mfumuyo idaimirira pa nsanja yake, ndipo idachita chipangano pamaso pa Chauta kuti idzatsata njira za Chauta, ndipo kuti idzasunga mau, malamulo ndi malangizo ake ndi mtima wake wonse ndiponso ndi moyo wake wonse, ndipo kuti idzagwiritsa ntchito mau a chipangano chimenechi monga momwe adalembedwera m'bukulo. Tsono anthu onse nawonso adavomera kutsata chipanganocho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Niima mfumu pachiunda, nichita pangano pamaso pa Yehova, kutsata Yehova ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukhazikitsa mau a chipangano cholembedwa m'buku ili; ndipo anthu onse anaimiririra panganoli.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inayimirira pambali pa chipilala ndi kuchita pangano pamaso pa Yehova kuti idzatsatira Yehova ndi kusunga malamulo, mawu ndi malangizo ake ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukwaniritsa mawu a mʼpanganoli, olembedwa mʼbukuli. Pamenepo anthu onse anadzipereka kutsatira panganoli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Niima mfumu paciunda, nicita pangano pamaso pa Yehova, kutsata Yehova, ndi kusunga malamulo ace, ndi mboni zace, ndi malemba ace, ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukhazikitsa mau a cipangano colembedwa m'buku ili; ndipo anthu onse anaimiririra panganoli.