2 Kings 23:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo nduna zake zidamnyamulira pa galeta kuchokera ku Medigo, nkupita naye ku Yerusalemu, ndipo zidamuika m'manda akeake. Kenaka anthu a ku Yuda adatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya namdzoza, ndipo iyeyo adaloŵa ufumu m'malo mwa bambo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anyamata ake anamtengera wakufa m'galeta, nabwera naye ku Yerusalemu kuchokera ku Megido, namuika m'manda akeake. Ndipo anthu a m'dziko anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya, namdzoza, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atumiki a Yosiyayo ananyamula mtembo wake mu galeta kuchokera ku Megido mpaka ku Yerusalemu ndipo anamuyika mʼmanda akeake. Ndipo anthu a mʼdzikomo anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya namudzoza, ndipo iye analowa ufumu mʼmalo mwa abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anyamata ace anamtengera wakufa m'gareta, nabwera naye ku Yerusalemu kucokera ku Megido, namuika m'manda ace ace. Ndipo anthu a m'dziko anatenga Yoahazi mwana wa Yosiya, namdzoza, namlonga ufumu m'malo mwa atate wace. Yoahazi, Yoyakimu ndi Yoyakini mafumu oipa a Yuda.