2 Kings 23:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yehowahazi anali wa zaka 23 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira miyezi itatu ku Yerusalemu. Mai wake anali Hamutala, mwana wa Yeremiya wa ku Libina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehowahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu miyezi itatu m'Yerusalemu ndi dzina la make ndiye Hamutala mwana wa Yeremiya wa ku Libina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehowahazi anakhala mfumu ali ndi 23 ndipo analamulira mu Yerusalemu miyezi itatu. Amayi ake anali Hamutali, mwana wa Yeremiya wa ku Libina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yoahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu miyezi itatu m'Yerusalemu ndi dzina la mace ndiye Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina.