2 Kings 23:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Farao Neko adamuika m'ndende ku Ribula m'dziko la Hamati, kuti asalamulirenso ku Yerusalemu. Pambuyo pake Faraoyo adaŵakhometsa msonkho wa siliva wolemera makilogramu 3,400, ndiponso golide wolemera makilogramu 34.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Farao Neko anammanga m'Ribula, m'dziko la Hamati; kuti asachite ufumu m'Yerusalemu; nasonkhetsa dzikoli msonkho wa matalente zana limodzi la siliva, ndi talente limodzi la golide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Farao Neko anamuyika mʼndende ku Ribula mʼdziko la Hamati kuti asalamulirenso mu Yerusalemu. Farao analamula Yuda kuti azikhoma msonkho wa siliva wolemera makilogalamu 3,400, ndiponso golide wolemera makilogalamu 34.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Faraoneko anammanga m'Ribila, m'dziko la Hamati; kuti asacite ufumu m'Yerusalemu; nasonkhetsa dzikoli msonkho wa matalente zana limodzi la siliva, ndi talente limodzi la golidi.